Pofuna kuonetsesa kuti mafuta a galimoto maaka diesel akupezeka m’malo onse omwetsera mafuta m’dziko muno, bungwe la National Oil Company of Malawi (NOCMA) lati galimoto 40 zonyamula mafuta tsopano zafika m’dziko muno kuchokera ku doko la Beira m’dziko la Mozambique.
Malinga ndi Mkulu nkhani ku bungwe la NOCMA, a Raymond Likambale, atinso panopa galimoto zina zokwana 70 zatenga kale mafuta a diesel ndipo zinyamuka ku Beira nthawi ili yonse ulendo obwera ku Malawi.
Poonjezera apo palinso sitima ina yapa mtunda yomwe yapita ku Nacala kukanyamula diesel okwana malita 1.6 million kuonjezera pa sitima ina yomwe yatsitsa kale malita ena 1 million ku malo osungila mafuta ku Matindi m’boma la Blantyre,” atero a Likambale.
Iwo ati pamene galimoto zikunyamula mafutawa ku Beira mdziko la Mozambique, zinanso zikunyamula mafuta ku Tanzania, ndipo pali chiyembekezo choti mafuta ayambanso kupezeka mosavuta masiku angapo akudzawa.
Comments